Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Luka 3:3 - Buku Lopatulika Ndipo iye anadza kudziko lonse la m'mbali mwa Yordani, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anadza kudziko lonse la m'mbali mwa Yordani, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Yohaneyo adayendera dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yordani, akulalika. Ankauza anthu kuti, “Tembenukani mtima ndi kubatizidwa, kuti Mulungu akukhululukireni machimo anu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anapita ku dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yorodani, nalalikira ubatizo wa kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo. |
Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordani, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu
Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Yordani, amene munamchitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye.
Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Yesu.
Ndipo tsopano uchedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuitane pa dzina lake.