Awa ndi malongosoledwe ao mu utumiki wao kulowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa chiweruzo adawapatsa Aroni atate wao, monga Yehova Mulungu wa Israele anamlamulira.
Luka 1:8 - Buku Lopatulika Ndipo panali, pakuchita iye ntchito yakupereka nsembe m'dongosolo la gulu lake, pamaso pa Mulungu, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali, pakuchita iye ntchito yakupereka nsembe m'dongosolo la gulu lake, pamaso pa Mulungu, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lina Zakariya ankagwira ntchito yake yaunsembe pamaso pa Mulungu. Inali nthaŵi ya gulu lake la ansembe kutumikira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi yogwira ntchito yotumikira ansembe a gulu la Zekariya, Zekariya ankatumikira ngati wansembe pamaso pa Mulungu, |
Awa ndi malongosoledwe ao mu utumiki wao kulowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa chiweruzo adawapatsa Aroni atate wao, monga Yehova Mulungu wa Israele anamlamulira.
Koma Nadabu ndi Abihu anafa, atate wao akali ndi moyo, opanda ana; momwemo Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe.
Pakuti Alevi anasiya podyetsa pao, ndi maiko aoao, nadza ku Yuda ndi ku Yerusalemu; popeza Yerobowamu ndi ana ake anawataya, kuti asachitire Yehova ntchito ya nsembe;
panalinso amuna mwa ana a Aroni ansembe, okhala m'minda ya kubusa kwa mizinda yao, m'mzinda uliwonse, otchulidwa maina ao, agawire amuna onse mwa ansembe, ndi onse mwa Alevi, oyesedwa mwa chibadwidwe magawo ao.
Ndipo Hezekiya anaika zigawo za ansembe ndi Alevi, monga mwa magawidwe ao, yense monga mwa utumiki wake, ndi ansembe ndi Alevi, achite nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika kutumikira, ndi kuyamika, ndi kulemekeza, kuzipata za chigono cha Yehova.
Ndipo anaika monga mwa chiweruzo cha Davide atate wake zigawo za ansembe ku utumiki wao, ndi Alevi ku udikiro wao, kulemekeza Mulungu, ndi kutumikira pamaso pa ansembe, monga munayenera tsiku ndi tsiku; odikira omwe monga mwa zigawo zao ku chipata chilichonse; pakuti momwemo Davide munthu wa Mulungu adamuuza.
Naika ansembe m'magawo mwao, ndi Alevi m'magawidwe mwao, atumikire Mulungu wokhala ku Yerusalemu, monga mulembedwa m'buku la Mose.
Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.
Ndipo uveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ake omwe; ndi kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andichitire Ine ntchito ya nsembe.
Ichi ndicho uwachitire kuwapatula, andichitire ntchito ya nsembe: tenga ng'ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo zangwiro,
Ndipo ndidzapatula chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; ndidzapatulanso Aroni ndi ana ake aamuna omwe, andichitire ntchito ya nsembe.
Uwamangirenso Aroni ndi ana ake aamuna mipango m'chuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi dzanja la ana ake aamuna.
Ndipo iwe ndi ana ako aamuna pamodzi ndi iwe muchite ntchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsalu yotchinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani ntchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.
Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana aakazi a fuko la Aroni, dzina lake Elizabeti.