Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 30:30 - Buku Lopatulika

30 Ndipo udzoze Aroni ndi ana ake aamuna, ndi kuwapatula andichitire ntchito ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Ndipo udzoze Aroni ndi ana ake amuna, ndi kuwapatula andichitire ntchito ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Kenaka udzamdzoze Aroni pamodzi ndi ana ake, ndi kuŵapatula kuti akhale ansembe onditumikira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 “Udzoze Aaroni ndi ana ake aamuna ndi kuwapatula kuti akhale ansembe onditumikira.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 30:30
11 Mawu Ofanana  

Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake.


Ndipo ulankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zovala apatulidwe nazo, andichitire Ine ntchito ya nsembe.


Ndipo uveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ake omwe; ndi kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andichitire Ine ntchito ya nsembe.


Ndipo uzipatule, kuti zikhale zopatulika ndithu; zonse zakuzikhudza zidzakhala zopatulika.


Nulankhule ndi ana a Israele, ndi kuti, Awa ndi mafuta odzoza opatulika a Ine mwa mibadwo yanu.


nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andichitire ntchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao.


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete.


Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula.


Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala paguwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna omwe; napatula Aroni, ndi zovala zake, ndi ana ake aamuna, ndi zovala za ana ake aamuna omwe.


Awa ndi maina a ana aamuna a Aroni, ansembe odzozedwawo, amene anawadzaza manja ao achite ntchito ya nsembe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa