Luka 1:18 - Buku Lopatulika Ndipo Zekariya anati kwa mngelo, Ndidzadziwitsa ichi ndi chiyani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zake za mkazi wanga zachuluka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Zekariya anati kwa mngelo, Ndidzadziwitsa ichi ndi chiyani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zake za mkazi wanga zachuluka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zakariya adafunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingadziŵe bwanji kuti zimenezi nzoona? Ineyo ndine nkhalamba, mkazi wanga nayenso wakalamba.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zakariya anamufunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingatsimikize bwanji zimenezi? Ine ndine wokalamba ndipo mkazi wanga ali ndi zaka zambiri.” |
Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala?
ndipo Sara anaseka m'mtima mwake, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba?
Pamenepo kazembe amene mfumu ankatsamira padzanja lake anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angachite mazenera m'mwamba chidzachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai.
Ndipo iye osafooka m'chikhulupiriro sanalabadire thupi lake, ndilo longa ngati lakufa pamenepo, (pokhala iye ngati zaka makumi khumi), ndi mimba ya Sara idaumanso;