Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 18:12 - Buku Lopatulika

12 ndipo Sara anaseka m'mtima mwake, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 ndipo Sara anaseka m'mtima mwake, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Motero Sara adangoseka, namati, “Ha, monga ndakalambira inemu, kodi nkuthekanso kuti ndikondwe ndi mwamuna wanga? Komanso mwamuna wanga ndi wokalamba zedi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Choncho anangoseka nati mu mtima mwake, “Kodi munthu wothayitha ngati ine ndingasangalalenso kugona pamodzi ndi mbuye wanga? Mwamuna wanga nayenso ndi wokalamba.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 18:12
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala?


Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba?


Ndipo anati, Nyengo ino chaka chikudzachi udzafukata mwana wamwamuna. Koma anati, Iai, mbuyanga, munthu wa Mulungu, musanamiza mdzakazi wanu.


Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, ndi lilime lathu linafuula mokondwera; pamenepo anati kwa amitundu, Yehova anawachitira iwo zazikulu.


potero mfumuyo adzakhumba kukoma kwako, pakuti ndiye mbuye wako; ndipo iwe umgwadire iye.


Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.


monga Sara anamvera Abrahamu, namutcha iye mbuye; ameneyo mukhala ana ake ngati muchita bwino, osaopa choopsa chilichonse.


Nadza mkaziyo, kutacha, nagwa pakhomo pa nyumba ya munthu padali mbuye wake, kufikira kutayera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa