Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m'chingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe.
Genesis 7:1 - Buku Lopatulika Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi akunyumba ako onse m'chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi akunyumba ako onse m'chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauza Nowa kuti, “Loŵa m'chombo iwe pamodzi ndi banja lako. Iwe wekha ndakupeza kuti ndiwe wochita zondikondweretsa mu mbadwo uno. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yehova anati kwa Nowa, “Lowa mu chombo iwe ndi banja lako lonse, chifukwa ndaona kuti ndiwe wolungama mu mʼbado uwu. |
Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m'chingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe.
Mibadwo ya Nowa ndi iyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m'mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.
Tsiku lomwelo analowa m'chingalawamo Nowa, ndi Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti, ana a Nowa, ndi mkazi wake wa Nowa, ndi akazi atatu a ana ake pamodzi nao:
Ndipo analowa Nowa ndi ana ake ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake m'chingalawamo, chifukwa cha madzi a chigumula.
chinkana akadakhala m'mwemo anthu awa atatu, Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadapulumutsa moyo wao wokha mwa chilungamo chao, ati Ambuye Yehova.
Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m'dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.
Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.
Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.
Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.
imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka chingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;