Genesis 7:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Ndipo Yehova anati kwa Nowa, “Lowa mu chombo iwe ndi banja lako lonse, chifukwa ndaona kuti ndiwe wolungama mu mʼbado uwu. Onani mutuwoBuku Lopatulika1 Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi akunyumba ako onse m'chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi akunyumba ako onse m'chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Chauta adauza Nowa kuti, “Loŵa m'chombo iwe pamodzi ndi banja lako. Iwe wekha ndakupeza kuti ndiwe wochita zondikondweretsa mu mbadwo uno. Onani mutuwo |