Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 7:2 - Buku Lopatulika

2 Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yamphongo ndi yaikazi yake; ndi nyama zosadyedwa ziwiriziwiri yamphongo ndi yaikazi yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yamphongo ndi yaikazi yake; ndi nyama zosadyedwa ziwiriziwiri yamphongo ndi yaikazi yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsono tenga magulu asanu ndi aŵiri a nyama, ziŵiriziŵiri, yaimuna ndi yaikazi, zimene amaperekera nsembe, ndipo utengenso nyama ziŵiriziŵiri, yaimuna ndi yaikazi, zosaperekera nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Pa mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya utengepo zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi zazikazi zisanu ndi ziwirinso. Koma pa mtundu wa nyama iliyonse yosati nʼkudya utengepo zazimuna ziwiri ndi zazikazi ziwirinso.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 7:2
9 Mawu Ofanana  

Ndiponso mbalame za kumlengalenga zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yaimuna ndi yaikazi, kuti mbeu ikhale ndi moyo padziko lonse lapansi.


Nyama zodyedwa ndi nyama zosadyedwa, ndi mbalame, ndi zonse zokwawa pansi,


Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo.


Ndipo aziphunzitsa anthu anga asiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi kuwazindikiritsa pakati pa zodetsa ndi zoyera.


ndi kuti musiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi pakati pa zodetsedwa ndi zoyera;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa