Ndipo Leya anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Rubeni; pakuti anati, Chifukwa kuti Yehova waona kuvutika kwanga ndipo tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine.
Genesis 49:3 - Buku Lopatulika Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi chiyambi cha mphamvu yanga; ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi chiyambi cha mphamvu yanga; ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Rubeni mwana wanga wachisamba, ndiwe nkhongono zanga, ndiwe mphatso yoyamba ya mphamvu zanga. Mwa ana anga onse, wopambana ndiwe pa ulemerero ndi mphamvu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Rubeni, ndiwe woyamba kubadwa; mphamvu yanga ndiponso chizindikiro choyamba cha mphamvu zanga, wopambana pa ulemerero ndi mphamvu. |
Ndipo Leya anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Rubeni; pakuti anati, Chifukwa kuti Yehova waona kuvutika kwanga ndipo tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine.
Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:
ana aamuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara;
Maina a ana a Israele amene anadza mu Ejipito ndi awa: Yakobo ndi ana aamuna ake: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo.
Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Msatero atate wanga, chifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pamutu wake.
Ndipo ana a Rubeni mwana woyamba wa Israele, (pakuti ndiye mwana woyamba; koma popeza anaipsa kama wa atate wake ukulu wake unapatsidwa kwa ana a Yosefe mwana wa Israele, koma m'buku la chibadwidwe asayesedwe monga mwa ukulu wake.
Ndi m'malire a Efuremu, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Rubeni, limodzi.
Ndipo ana a Rubeni, mwana woyamba wa Israele, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina mmodzimmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israele; ana aamuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu;
Koma azivomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lake la zake zonse; popeza iye ndiye chiyambi cha mphamvu yake; zoyenera woyamba kubadwa nzake.
Naimirire awa paphiri la Ebala, kutemberera: Rubeni, Gadi, ndi Asere, ndi Zebuloni, Dani ndi Nafutali.
Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Laodikea lemba: Izi anena Ameni'yo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu: