Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 5:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo ana a Rubeni mwana woyamba wa Israele, (pakuti ndiye mwana woyamba; koma popeza anaipsa kama wa atate wake ukulu wake unapatsidwa kwa ana a Yosefe mwana wa Israele, koma m'buku la chibadwidwe asayesedwe monga mwa ukulu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo ana a Rubeni mwana woyamba wa Israele, (pakuti ndiye mwana woyamba; koma popeza anaipsa kama wa atate wake ukulu wake unapatsidwa kwa ana a Yosefe mwana wa Israele, koma m'buku la chibadwidwe asayesedwe monga mwa ukulu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Naŵa ana a Rubeni, mwana wachisamba wa Israele. Inde Rubeni analidi mwana wachisamba, koma chifukwa adaagona ndi mkazi wina wamng'ono wa bambo wake, uchisamba wakewo udapatsidwa kwa Yosefe, mng'ono wake. Motero Rubeniyo saoneka pa mndandanda wa maina potsata za kubadwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli (iye anali woyamba kubadwa, koma atagona ndi mkazi wamngʼono wa abambo ake, ulemu wake wokhala mwana woyamba unaperekedwa kwa ana a Yosefe. Kotero iye sanalembedwe pa mndandanda wa mayina ngati mwana woyamba kubadwa,

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 5:1
23 Mawu Ofanana  

Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri ili m'mimba mwako, magulu awiri a anthu adzatuluka m'mimba mwako; gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake; wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.


Ndipo Yakobo anati, Tigulane lero ukulu wako.


Ndipo Leya anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Rubeni; pakuti anati, Chifukwa kuti Yehova waona kuvutika kwanga ndipo tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine.


Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:


Maina a ana a Israele amene anadza mu Ejipito ndi awa: Yakobo ndi ana aamuna ake: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo.


Tsopano ana ako aamuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Ejipito, ndisanadze kwa iwe ku Ejipito, ndiwo anga; Efuremu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.


Ana a Israele ndi awa: Rubeni, Simeoni, Levi, ndi Yuda, Isakara, ndi Zebuloni,


Hosa yemwe wa ana a Merari anali ndi ana, wamkulu ndi Simiri; pakuti ngakhale sanali wobadwa woyamba, atate wake anamuyesa wamkulu;


Akulu a mbumba za makolo ao ndi awa: ana aamuna a Rubeni, woyamba wa Israele ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi; amenewo ndiwo mabanja a Rubeni.


Usamavula mkazi wa atate wako; ndiye thupi la atate wako.


Munthu akagona naye mkazi wa atate wake, wavula atate wake; awaphe ndithu onse awiri; mwazi wao ukhale pamutu pao.


Ndipo maina a amuna amene aime nanu ndi awa: wa Rubeni, Elizuri mwana wa Sedeuri.


Koma Kora, mwana wa Izihara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni;


Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israele; ana aamuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu;


Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati panu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.


Koma azivomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lake la zake zonse; popeza iye ndiye chiyambi cha mphamvu yake; zoyenera woyamba kubadwa nzake.


Wotembereredwa iye wakugona ndi mkazi wa atate wake; popeza wavula atate wake. Ndi anthu onse anene, Amen.


Woyamba kubadwa wa ng'ombe yake, ulemerero ndi wake; nyanga zake ndizo nyanga zanjati; adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi. Iwo ndiwo zikwi khumi za Efuremu, iwo ndiwo zikwi za Manase.


amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse;


Pamenepo ana a Yuda anadza kwa Yoswa ku Giligala; ndi Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi ananena naye, Mudziwa chimene Yehova adanena kwa Mose munthu wa Mulungu za ine ndi za inu mu Kadesi-Baranea.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa