Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 46:8 - Buku Lopatulika

8 Maina a ana a Israele amene anadza mu Ejipito ndi awa: Yakobo ndi ana aamuna ake: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Maina a ana a Israele amene anadza m'Ejipito ndi awa: Yakobo ndi ana amuna ake: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Naŵa maina a Aisraele amene adapita ku Ejipito, ndiye kuti Yakobe ndi ana ake. Rubeni, mwana wachisamba wa Yakobe,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Nawa ana a Israeli (ndiye kuti Yakobo ndi ana ake) amene anapita ku Igupto: Rubeni mwana woyamba wa Yakobo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 46:8
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Leya anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Rubeni; pakuti anati, Chifukwa kuti Yehova waona kuvutika kwanga ndipo tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine.


ana ake aamuna, ndi zidzukulu zake zazimuna, ndi ana aakazi ake, ndi zidzukulu zake zazikazi, ndi mbeu zake zonse anadza nazo mu Ejipito.


Ndi ana aamuna a Rubeni: Hanoki, ndi Palu, ndi Hezironi, ndi Karimi.


Ndipo maina a amuna amene aime nanu ndi awa: wa Rubeni, Elizuri mwana wa Sedeuri.


Rubeni akhale ndi moyo, asafe, koma amuna ake akhale owerengeka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa