Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 46:7 - Buku Lopatulika

7 ana ake aamuna, ndi zidzukulu zake zazimuna, ndi ana aakazi ake, ndi zidzukulu zake zazikazi, ndi mbeu zake zonse anadza nazo mu Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 ana ake amuna, ndi zidzukulu zake zazimuna, ndi ana akazi ake, ndi zidzukulu zake zazikazi, ndi mbeu zake zonse anadza nazo m'Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 ndiye kuti ana ndi adzukulu ake aamuna, ndiponso ana ndi adzukulu ake aakazi. Onsewo adapita nawo ku Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndiye kuti popita ku Igupto Yakobo anatenga ana aamuna, zidzukulu zazimuna, ana aakazi ndi zidzukulu zazikazi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 46:7
9 Mawu Ofanana  

Ndipo pakumva icho ana ake aamuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anapwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israele pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita.


Ndipo anatenga ng'ombe zao ndi chuma chao anachipeza m'dziko la Kanani, nadza ku Ejipito, Yakobo ndi mbeu zake zonse pamodzi ndi iye;


Maina a ana a Israele amene anadza mu Ejipito ndi awa: Yakobo ndi ana aamuna ake: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo.


Pamenepo Israele analowa mu Ejipito; ndi Yakobo anakhala mlendo m'dziko la Hamu.


Pakuti Ambuye Yehova atero, Anthu anga ananka ku Ejipito poyamba paja, kukakhala kumeneko; ndipo Asiriya anawatsendereza popanda chifukwa.


kuti makolo athu anatsikira kunka ku Ejipito, ndipo tinakhala mu Ejipito masiku ambiri; ndipo Aejipito anachitira zoipa ife, ndi makolo athu.


Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m'dziko lake.


Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye Mwaramu wakuti atayike, natsika kunka ku Ejipito, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang'ono, nasandukako mtundu waukulu, wamphamvu, ndi wochuluka anthu ake;


Ndi kwa Isaki ndinapatsa Yakobo ndi Esau, ndipo ndinampatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake; koma Yakobo ndi ana ake anatsikira kunka ku Ejipito.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa