Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wachinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe.
Genesis 48:22 - Buku Lopatulika Ndipo ine ndakupatsa iwe gawo limodzi loposa la abale ako, limene ndinalanda m'dzanja la Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ine ndakupatsa iwe gawo limodzi loposa la abale ako, limene ndinalanda m'dzanja la Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiponso iweyo, osati abale ako, ndikukupatsa Sekemu, dera lija limene ndidachita cholanda ndi lupanga langa ndi uta wanga kwa Aamori.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndiponso iwe wekha ndikupatsa moposera abale ako, malo woonjezera, Sekemu, malo amene ndinalanda kwa Aamori ndi lupanga ndi uta wanga.” |
Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wachinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe.
Ndipo anagula ndi ndalama zana limodzi dera la munda kumeneko anamanga hema wake, padzanja la ana ake a Hamori atate wake wa Sekemu.
Ndipo analanda nkhosa zao ndi zoweta zao ndi abulu ao, ndi za m'mzinda, ndi za m'munda;
Pakuti Yuda anakula mphamvu mwa abale ake, ndi mtsogoleri anafuma kwa iyeyu, koma ukulu ngwa Yosefe);
Atero Ambuye Yehova, Malire amene mugawe nao dziko likhale cholowa chao monga mwa mafuko khumi ndi awiri a Israele ndi awa: Yosefe akhale nao magawo awiri.
Koma ndinaononga Ine pamaso pa Aamori, amene msinkhu wao unanga msinkhu wa mikungudza, nakhala nayo mphamvu ngati thundu; koma ndinaononga zipatso zao m'mwamba, ndi mizu yao pansi.
Chifukwa chake anadza kumzinda wa Samariya, dzina lake Sikari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe;
Koma azivomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lake la zake zonse; popeza iye ndiye chiyambi cha mphamvu yake; zoyenera woyamba kubadwa nzake.
Ndipo mafupa a Yosefe amene ana a Israele anakwera nao kuchokera ku Ejipito anawaika ku Sekemu, pa kadziko kamene adakagula Yakobo kwa ana a Hamori atate wa Sekemu ndi kuwapatsa ndalama zana; ndipo anakhala cholowa cha ana a Yosefe.
Motero Yehova Mulungu wa Israele anaingitsa Aamori, pamaso pa anthu ake Israele, ndipo kodi liyenera kukhala cholowa chanu?