Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 4:5 - Buku Lopatulika

5 Chifukwa chake anadza kumzinda wa Samariya, dzina lake Sikari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Chifukwa chake anadza kumudzi wa Samariya, dzina lake Sikari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsono adafika ku mudzi wina wa ku Samariya, dzina lake Sikari, pafupi ndi kadziko kamene Yakobe adaapatsa Yosefe, mwana wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Iye anafika mʼmudzi wa Asamariya wotchedwa Sukari, pafupi ndi malo amene Yakobo anapatsa mwana wake Yosefe.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 4:5
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anagula ndi ndalama zana limodzi dera la munda kumeneko anamanga hema wake, padzanja la ana ake a Hamori atate wake wa Sekemu.


Ndipo ine ndakupatsa iwe gawo limodzi loposa la abale ako, limene ndinalanda m'dzanja la Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga.


Popeza mau aja anawafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe la ku Betele, ndi kutemberera nyumba zonse za misanje ili m'mizinda ya ku Samariya, adzachitika ndithu.


natumiza amithenga patsogolo pake; ndipo ananka, nalowa m'mudzi wa Asamariya, kukamkonzera Iye malo.


Kodi muli wamkulu ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife chitsimechi, namwamo iye yekha, ndi ana ake, ndi zoweta zake?


Ndipo m'mzinda muja anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira Iye chifukwa cha mau a mkazi, wochita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu zilizonse ndinazichita.


ndipo pamenepo panali chitsime cha Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wake, motero anakhala pachitsime.


Pakuti ophunzira ake adachoka kunka kumzinda kuti akagule chakudya.


Ndipo mafupa a Yosefe amene ana a Israele anakwera nao kuchokera ku Ejipito anawaika ku Sekemu, pa kadziko kamene adakagula Yakobo kwa ana a Hamori atate wa Sekemu ndi kuwapatsa ndalama zana; ndipo anakhala cholowa cha ana a Yosefe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa