Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,
Genesis 48:12 - Buku Lopatulika Ndipo Yosefe anatulutsa iwo pakati pa maondo ake, nawerama ndi nkhope yake pansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yosefe anatulutsa iwo pakati pa maondo ake, nawerama ndi nkhope yake pansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yosefe adatenga anawo kuŵachotsa pa maondo a Yakobe. Ndipo adamgwadira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Yosefe anawachotsa ana aja pa mawondo a Israeli ndipo anamuweramira nkhope pansi. |
Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,
Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake.
Ndipo iye mwini anatsogolera patsogolo pao, nawerama pansi kasanu ndi kawiri mpaka anayandikira mkulu wake.
Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.
Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Sindinaganizira kuti ndiona nkhope yako: ndipo, taona, Mulungu wandionetsa ine mbeu zako zomwe.
Ndipo Yosefe anatenga iwo onse awiri, Efuremu m'dzanja lake lamanja ku dzanja lamanzere la Yakobo, ndi Manase m'dzanja lake lamanzere ku dzanja lamanja la Israele, nadza nao pafupi ndi iye.
Tsono Bateseba ananka kwa mfumu Solomoni kukanenera Adoniya kwa iye. Ndipo mfumu inanyamuka kukomana naye, namuweramira nakhalanso pa mpando wake wachifumu, naikitsa mpando wina wa amake wa mfumu, nakhala iye ku dzanja lake lamanja.
Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Aliyense aope mai wake, ndi atate wake; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako; Ine ndine Yehova.