Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi;
Genesis 47:10 - Buku Lopatulika Ndipo Yakobo anamdalitsa Farao, natuluka pamaso pa Farao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yakobo anamdalitsa Farao, natuluka pamaso pa Farao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo atadalitsa Farao, adatsazikana naye nkuchokapo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atatha kumudalitsa Farao uja, Yakobo anatsanzika nʼkunyamuka. |
Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi;
Ndipo Yosefe anakhazika atate wake ndi abale ake, napatsa iwo pokhala m'dziko la Ejipito, m'dera lokometsetsa la m'dziko, m'dziko la Ramsesi, monga analamulira Farao.
Ndipo Yosefe analowa naye Yakobo atate wake, namuika iye pamaso pa Farao; ndipo Yakobo anamdalitsa Farao.
Ndipo anthu onse anaoloka Yordani, ndi mfumu yomwe inaoloka; ndipo mfumuyo inapsompsona Barizilai nimdalitsa; ndipo iye anabwerera kunka kumalo kwake.
Toi anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide, kuti akamlonjere ndi kumdalitsa, popeza anamenyana ndi Hadadezere ndi kumkantha; pakuti pakati pa Hadadezere ndi Toi panali nkhondo. Ndipo Yoramu anabwera ndi zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolide, ndi zotengera zamkuwa.
Angakhale opitirirapo sanena, Dalitso la Mulungu likhale pa inu; tikudalitsani m'dzina la Yehova.
Pamenepo Yoswa anamdalitsa, napatsa Kalebe mwana wa Yefune Hebroni likhale cholowa chake.
Ndipo taona, Bowazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa ocheka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni.