Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 7:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo popanda chitsutsano konse wamng'ono adalitsidwa ndi wamkulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo popanda chitsutsano konse wamng'ono adalitsidwa ndi wamkulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Paja nchodziŵikiratu kuti munthu wodalitsa mnzake ndiye wamkulu kuposa amene akudalitsidwayo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mosakayika konse, munthu amene amadalitsa ndi wamkulu kuposa amene akudalitsidwayo.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 7:7
16 Mawu Ofanana  

Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israele: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wake anawadalitsa.


Pamenepo Davide anabwerera kudalitsa nyumba yake. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anatulukira kwa Davide, nati; Ha! Lero mfumu ya Israele inalemekezeka ndithu, amene anavula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ake, monga munthu woluluka avula wopanda manyazi!


Naimirira, nadalitsa msonkhano wonse wa Israele ndi mau okweza, nati,


Pamenepo ansembe Alevi anauka, nadalitsa anthu; ndi mau ao anamveka, ndi pemphero lao lidakwera pokhala pake popatulika Kumwamba.


Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.


Kumwamba kutchere khutu, ndipo ndidzanena; ndi dziko lapansi limve mau a m'kamwa mwanga.


Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.


koma iye amene mawerengedwe a chibadwidwe chake sachokera mwa iwo, anatenga limodzi la magawo khumi kwa Abrahamu, namdalitsa iye amene ali nao malonjezano.


Ndipo pano anthu ofeka alandira limodzi la magawo khumi; koma apo iye, woti adamchitira umboni kuti ali ndi moyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa