Ndipo panali zitapita izi, wopereka chikho wa mfumu ya Aejipito ndi wophika mkate wake anamchimwira mbuye wao mfumu ya Aejipito.
Genesis 40:2 - Buku Lopatulika Ndipo Farao anakwiyira akulu ake awiriwo wamkulu wa opereka chikho, ndi wamkulu wa ophika mkate. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Farao anakwiyira akulu ake awiriwo wamkulu wa opereka chikho, ndi wamkulu wa ophika mkate. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Farao adaŵakwiyira kwambiri antchito ake aŵiriwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Farao anapsa mtima ndi akuluakulu awiriwa, |
Ndipo panali zitapita izi, wopereka chikho wa mfumu ya Aejipito ndi wophika mkate wake anamchimwira mbuye wao mfumu ya Aejipito.
Ndipo anabwezanso wopereka chikho ku ntchito yake; ndipo iye anapereka chikho m'manja a Farao.
Farao anakwiya ndi anyamata ake, nandiika ine ndisungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, ine ndi wophika mkate wamkulu:
ndi woyang'anira minda yampesa ndiye Simei Mramati; ndi woyang'anira zipatso za minda yampesa zisungike mosungiramo vinyo ndiye Zabidi Msifamu;
Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.
Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango; koma kukoma mtima kwake kunga mame pamsipu.
Koma Herode anaipidwa nao a ku Tiro ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasito mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zochokera ku dziko la mfumu.