Machitidwe a Atumwi 12:20 - Buku Lopatulika20 Koma Herode anaipidwa nao a ku Tiro ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasito mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zochokera ku dziko la mfumu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Koma Herode anaipidwa nao a ku Tiro ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasito mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zochokera ku dziko la mfumu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Herode adaaŵakwiyira anthu a ku Tiro ndi a ku Sidoni. Tsono anthuwo adadza pamodzi kwa iye. Adaayamba akopa Blasito, kapitao wa ku nyumba ya mfumu kenaka nkukapempha mtendere, chifukwa chakudya cha m'dziko laolo chinkachokera m'dziko la mfumuyo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Herode anakwiyira anthu a ku Turo ndi Sidoni; anthuwo anagwirizana zoti akambirane naye. Atapeza thandizo kuchokera kwa Blasito, wantchito wokhulupirika wa mfumu, anapempha kuti pakhale mtendere, chifukwa dziko lawo limadalira dziko la mfumuyo pa chakudya chawo. Onani mutuwo |