Genesis 4:12 - Buku Lopatulika pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ukamalima mbeu, nthakayo sidzakubalira, ndipo udzakhala womangoyendayenda, wosoŵa pokhala penipeni pa dziko lapansi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Udzalima munda koma nthakayo sidzakupatsanso zokolola zake. Udzakhala wosakhazikika; womangoyendayenda pa dziko lapansi.” |
Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.
Ana ake akhale amchirakuyenda ndi opemphapempha; afunefune zosowa zao kuchokera m'mabwinja mwao.
Mulungu wanga adzawataya, pakuti sanammvere Iye; ndipo adzakhala othawathawa mwa amitundu.
M'munda mwaonongeka, nthaka ilira; pakuti tirigu waonongeka, vinyo watsopano wamwelera, mafuta akudza pang'onong'ono.
Ndipo nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.
ndipo mudzachita nayo mphamvu yanu chabe; ndi nthaka yanu siidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'dziko siidzabala zobala zake.
Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.
Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha Iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo
Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani.