Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 4:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Udzalima munda koma nthakayo sidzakupatsanso zokolola zake. Udzakhala wosakhazikika; womangoyendayenda pa dziko lapansi.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

12 pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ukamalima mbeu, nthakayo sidzakubalira, ndipo udzakhala womangoyendayenda, wosoŵa pokhala penipeni pa dziko lapansi.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 4:12
16 Mawu Ofanana  

Kaini anati kwa Yehova, “Chilango changa ndi chachikulu kuposera mphamvu zanga.


Lero mukundipirikitsa pa dziko ndi pamaso panu; ndidzakhala wosakhazikika, woyendayenda, ndipo aliyense amene adzandipeze adzandipha.”


ndiponso nthaka yachonde kukhala nthaka yamchere, chifukwa cha kuyipa kwa amene amakhala kumeneko.


Ana ake akhale oyendayenda ndi opemphapempha; apirikitsidwe kuchoka pa mabwinja a nyumba zawo.


Munthu amene wapalamula mlandu wopha munthu adzakhala wothawathawa mpaka imfa yake; wina aliyense asamuthandize.


Mulungu wanga adzawakana chifukwa sanamumvere Iye; adzakhala oyendayenda pakati pa anthu a mitundu ina.


Minda yaguga, nthaka yauma; tirigu wawonongeka, vinyo watsopano watha, mitengo ya mafuta yauma.


Ndidzakufulatirani, kotero kuti adani anu adzakugonjetsani. Odana nanu adzakulamulirani ndipo inu muzidzagothawa popanda wokupirikitsani.


Mphamvu zanu zidzapita pachabe chifukwa nthaka yanu sidzabala kanthu, ngakhale mitengo yake sidzabala zipatso zake.


“ ‘Kunena za amene adzatsale, ndidzayika mantha mʼmitima mwawo mʼdziko la adani awo kotero kuti adzathawa ngakhale mtswatswa wa tsamba lowuluka ndi mphepo. Adzathawa ngati akuthawa lupanga, ndipo adzagwa pansi ngakhale padzakhale wopanda kuwapirikitsa.


Pakuti chilengedwe sichinasankhe kugonjera zopanda pake, koma mwachifuniro cha Iye amene analola kuti chigonjere. Koma chili ndi chiyembekezo


Koma ngati simumvera Yehova Mulungu wanu ndi kusatsata mosamalitsa malamulo ake ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsani lero lino, matemberero awa adzabwera pa inu ndikukugonjetsani:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa