Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 4:11 - Buku Lopatulika

11 Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, imene inatsegula pakamwa pake kulandira padzanja lako mwazi wa mphwako:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, imene inatsegula pakamwa pake kulandira pa dzanja lako mwazi wa mphwako:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsopano watembereredwa, sudzailimanso nthaka yomwe yamwa magazi a mng'ono wako, amene waŵakhetsa ndi manja ako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ndipo tsopano ndiwe wotembereredwa ndipo wachotsedwa mʼdziko limene nthaka yake inatsekula pakamwa pake kulandira magazi a mʼbale wako amene unakhetsa.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 4:11
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Chifukwa kuti wachita ichi, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m'thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya fumbi masiku onse a moyo wako:


Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.


namutcha dzina lake Nowa, ndi kuti, Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pantchito zathu zovuta za manja athu, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova;


Dziko iwe, usakwirire mwazi wanga, ndi kulira kwanga kusowe popumira.


Pakuti taonani, Yehova adza kuchokera kumalo ake kudzazonda okhala padziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake.


Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wosakhala m'zonse zolembedwa m'buku la chilamulo, kuzichita izi.


Ndipo dziko linathandiza mkaziyo, ndi dziko linatsegula m'kamwa mwake, nilinameza madzi a mtsinje amene chinjoka chinalavula m'kamwa mwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa