Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 109:10 - Buku Lopatulika

10 Ana ake akhale amchirakuyenda ndi opemphapempha; afunefune zosowa zao kuchokera m'mabwinja mwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ana ake akhale amchirakuyenda ndi opemphapempha; afunefune zosowa zao kuchokera m'mabwinja mwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ana ake azingoyendayenda nkumapemphapempha, apirikitsidwe m'mabwinja m'mene amakhala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ana ake akhale oyendayenda ndi opemphapempha; apirikitsidwe kuchoka pa mabwinja a nyumba zawo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 109:10
10 Mawu Ofanana  

chilango chigwere pamutu wa Yowabu ndi pa nyumba yonse ya atate wake; ndipo kusasoweke kunyumba ya Yowabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa chakudya.


Chifukwa chake khate la Naamani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako chikhalire. Ndipo anatuluka pamaso pake wakhate wa mbuu ngati chipale chofewa.


Akachuluka ana ake, ndiko kuchulukira lupanga, ndi ana ake sadzakhuta chakudya.


Ana ake akhala otekeseka, napsinjika kuchipata, wopanda wina wakuwapulumutsa.


Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenye wolungama atasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.


Ayendeyende ndi kufuna chakudya, nachezere osakhuta.


Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa