Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 39:12 - Buku Lopatulika

Ndipo mkazi anagwira iye chofunda chake, nati, Gona ndi ine; ndipo anasiya chofunda chake m'dzanja lake nathawa, natulukira kubwalo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo mkazi anagwira iye chofunda chake, nati, Gona ndi ine; ndipo anasiya chofunda chake m'dzanja lake nathawa, natulukira kubwalo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mkazi uja adamgwira mwinjiro Yosefeyo, namuuza kuti, “Ugone nane basi!” Koma iye adathaŵira pabwalo, kusiya mwinjiro uja uli m'manja mwa mkaziyo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mkazi uja anamugwira mkanjo Yosefe nati, “Tiye ugone nane!” Koma Yosefe anasiya mkanjo wake mʼmanja mwa mkaziyo nathawira kunja kwa nyumba.

Onani mutuwo



Genesis 39:12
16 Mawu Ofanana  

Ndipo pali pakunenanena ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, iye sanamvere mkazi kugona naye kapena kukhala naye.


Ndipo panali, nthawi yomweyo, iye analowa m'nyumba kuti agwire ntchito yake; ndipo munalibe amuna a m'nyumba m'katimo.


Ndipo panali pamene mkazi anaona kuti anasiya chofunda chake m'dzanja lake, nathawira kubwalo,


Koma iye anakana, nati kwa mkazi wa mbuyake, Taonani, mbuyanga sadziwa chimene chili ndi ine m'nyumbamu, ndipo anaika zake zonse m'manja anga;


Ndipo pamene anabwera nato pafupi kuti adye, iye anamgwira, nanena naye, Idza nugone nane, mlongo wanga.


Mwananga, usayende nao m'njira; letsa phazi lako ku mayendedwe ao;


Siyanitsa njira yako kutali kwa iyeyo, osayandikira ku khomo la nyumba yake;


Dzipulumutse wekha ngati mphoyo kudzanja la msaki, ndi mbalame kudzanja la msodzi.


ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wake ukunga maukonde, manja ake ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wochimwa adzagwidwa naye.


Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.


Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.


Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;


Ndipo pakupotoloka Samuele kuti achoke, iye anagwira chilezi cha mwinjiro wake, ndipo chinang'ambika.