Genesis 38:9 - Buku Lopatulika Ndipo Onani anadziwa kuti mbeu siidzakhala yake: ndipo panali pamene iye analowana naye mkazi wa mbale wake, kuti anaitaya pansi, kuti angampatse mbeu kwa mkulu wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Onani anadziwa kuti mbeu siidzakhala yake: ndipo panali pamene iye analowana naye mkazi wa mbale wake, kuti anaitaya pansi, kuti angampatse mbeu kwa mkulu wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Onani adaadziŵa kuti anawo sadzakhala ake. Motero nthaŵi zonse akamakhala naye mkaziyo, ankangotayira pansi mbeu yake, kuti asamubalire ana mbale wakeyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Onani anadziwa kuti mwanayo sadzakhala wake. Choncho nthawi zonse pamene amagona naye mkaziyo, ankatayira umuna pansi kuti asamuberekere mwana mʼbale wake. |
Abale akakhala pamodzi, nafa wina wa iwowa, wopanda mwana wamwamuna, mkazi wa wakufayo asakwatibwe ndi mlendo wakunja; mbale wa mwamuna wake alowane naye, namtenge akhale mkazi wake, namchitire zoyenera mbale wa mwamuna wake.
Ndipo kudzali, kuti woyamba kubadwa amene adzambala, adzalowa dzina lake la mbale wake wakufayo, kuti dzina lake lisafafanizidwe mu Israele.
Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.
Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi.
Pakuti pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali chisokonekero ndi chochita choipa chilichonse.
Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?
Nati Naomi, Bwererani, ana anga, mudzatsagana nane bwanji? Ngati ndili nao m'mimba mwanga ana aamuna ena kuti akhale amuna anu?
Ndiponso Rute Mmowabu, mkazi wa Maloni ndamgula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa cholowa chake; kuti dzina la wakufayo lisaiwalike pakati pa abale ake, ndi pa chipata cha malo ake; inu ndinu mboni lero lino.