Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Rute 1:11 - Buku Lopatulika

11 Nati Naomi, Bwererani, ana anga, mudzatsagana nane bwanji? Ngati ndili nao m'mimba mwanga ana aamuna ena kuti akhale amuna anu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Nati Naomi, Bwererani, ana anga, mudzatsagana nane bwanji? Ngati ndili nao m'mimba mwanga ana amuna ena kuti akhale amuna anu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Koma Naomi adaŵauza kuti, “Pepani ana anga, bwererani kwanu. Chifukwa chiyani mukufuna kupita nao? Kodi mukuganiza kuti ndingathe kubala ana ena aamuna, kuti adzakhale amuna anu?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma Naomi anati, “Bwererani kwanu ana anga. Chifukwa chiyani mukufuna kupita ndi ine? Kodi ine ndingaberekenso ana ena kuti akhale amuna anu?

Onani mutuwo Koperani




Rute 1:11
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpongozi wake, Khala wamasiye m'nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna: chifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ake. Ndipo Tamara ananka nakhala m'nyumba ya atate wake.


Ndipo Onani anadziwa kuti mbeu siidzakhala yake: ndipo panali pamene iye analowana naye mkazi wa mbale wake, kuti anaitaya pansi, kuti angampatse mbeu kwa mkulu wake.


Abale akakhala pamodzi, nafa wina wa iwowa, wopanda mwana wamwamuna, mkazi wa wakufayo asakwatibwe ndi mlendo wakunja; mbale wa mwamuna wake alowane naye, namtenge akhale mkazi wake, namchitire zoyenera mbale wa mwamuna wake.


Ndipo ananena naye, Iai, koma tidzapita nanu kwa anthu a kwanu.


Bwererani, ana anga, mukani, pakuti ndakalambitsa ine, sindingathe kukhala naye mwamuna. Ngakhale ndikati, Ndili nacho chiyembekezo, ndikhala naye mwamuna usiku uno, ndi kubalanso ana aamuna;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa