Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Rute 1:12 - Buku Lopatulika

12 Bwererani, ana anga, mukani, pakuti ndakalambitsa ine, sindingathe kukhala naye mwamuna. Ngakhale ndikati, Ndili nacho chiyembekezo, ndikhala naye mwamuna usiku uno, ndi kubalanso ana aamuna;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Bwererani, ana anga, mukani, pakuti ndakalambitsa ine, sindikhoza kukhala naye mwamuna. Ngakhale ndikati, Ndili nacho chiyembekezo, ndikhala naye mwamuna usiku uno, ndi kubalanso ana amuna;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Bwererani ana anga, muzipita kwanu, pakuti ndakalamba kwambiri, sindingathenso kukhala ndi mwamuna. Ngakhale ndikadanena kuti chikhulupiriro chilipobe, ngakhale ndikadakhala ndi mwamuna usiku uno, kuti ndibale ana aamuna,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Bwererani kwanu ana anga muzipita kwanu. Ine ndakalamba kwambiri kotero kuti sindingakwatiwenso. Ngakhale ndikananena kuti ndili nacho chikhulupiriro, ngakhale ndikanakhala ndi mwamuna usiku uno, ndipo nʼkubala ana aamuna,

Onani mutuwo Koperani




Rute 1:12
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala?


Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpongozi wake, Khala wamasiye m'nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna: chifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ake. Ndipo Tamara ananka nakhala m'nyumba ya atate wake.


Asawerengedwe wamasiye ngati sanafikire zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna mmodzi,


Nati Naomi, Bwererani, ana anga, mudzatsagana nane bwanji? Ngati ndili nao m'mimba mwanga ana aamuna ena kuti akhale amuna anu?


kodi mudzawalindirira akakula? Mudzadziletsa osakwatibwa? Iai, ana anga, pakuti chandiwawa koposa chifukwa cha inu popeza dzanja la Yehova landitulukira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa