Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Rute 1:13 - Buku Lopatulika

13 kodi mudzawalindirira akakula? Mudzadziletsa osakwatibwa? Iai, ana anga, pakuti chandiwawa koposa chifukwa cha inu popeza dzanja la Yehova landitulukira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 kodi mudzawalindirira akakula? Mudzadziletsa osakwatibwa? Iai, ana anga, pakuti chandiwawa koposa chifukwa cha inu popeza dzanja la Yehova landitulukira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 kodi tsono mukadatha kudikira mpaka akule? Kodi zimenezi zikadakuletsani kukwatiwa? Ai, ana anga, zotere zikadandiŵaŵa kwambiri chifukwa cha inu, poona kuti sindinu koma ndine amene Chauta adafuna kuti ndizunzike.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 kodi inu mukanadikira kuti akule? Kodi mukanakhalabe osakwatiwa kudikira iwowo? Ayi ana anga. Zimenezi zikundiwawa kwambiri kuposa inu, chifukwa ndi ineyo amene Yehova wafuna kuti ndizunzike.”

Onani mutuwo Koperani




Rute 1:13
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpongozi wake, Khala wamasiye m'nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna: chifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ake. Ndipo Tamara ananka nakhala m'nyumba ya atate wake.


Ndichitireni chifundo, ndichitireni chifundo, mabwenzi anga inu; pakuti dzanja la Mulungu landikhudza.


Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.


Pakuti mivi yanu yandilowa, ndi dzanja lanu landigwera.


Komanso dzanja la Yehova linatsutsana nao, kuwaononga m'chigono, kufikira adawatha.


Kuli konse anatuluka, dzanja la Yehova linawakhalira moipa, monga Yehova adanena, ndi monga Yehova adawalumbirira; nasautsika kwambiri iwowa.


Bwererani, ana anga, mukani, pakuti ndakalambitsa ine, sindingathe kukhala naye mwamuna. Ngakhale ndikati, Ndili nacho chiyembekezo, ndikhala naye mwamuna usiku uno, ndi kubalanso ana aamuna;


Nakweza iwo mau ao, naliranso misozi; ndi Oripa anampsompsona mpongozi wake, koma Rute anamkangamira.


Ndinachoka pano wolemera, nandibwezanso kwathu Yehova wopanda kanthu; munditcheranji Naomi, popeza Yehova wandichitira umboni wakunditsutsa, ndi Wamphamvuyonse wandichitira chowawa?


Chifukwa chake anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Chotsani likasa la Mulungu wa Israele, lipitenso kumalo kwake, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m'mzinda monse; dzanja la Mulungu linavutadi pamenepo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa