Ndipo anati mwamunayo, Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya.
Genesis 3:6 - Buku Lopatulika Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wopatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene anali naye, nadya iyenso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya iyenso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mkaziyo adaona kuti mtengowo ndi wokongola, ndiponso kuti zipatso zake zingakhale zokoma kudya. Pompo adayamba kukhumbira kuti adyeko zipatsozo, adzakhale wanzeru. Motero adathyolako zipatso zina za mtengowo, naadya. Tsono zina adapatsako mwamuna wake, ndipo iyenso adadya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene mkaziyo anaona kuti mtengowo unali wabwino kudya ndi wokongola ndi kuti unali wopatsa nzeru, anatengako zipatso zake nadya. Zina anamupatsako mwamuna wake amene anali naye pomwepo ndipo naye anadyanso. |
Ndipo anati mwamunayo, Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya.
Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mau a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m'kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako:
Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyake anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine.
kuti ana aamuna a Mulungu anayang'ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.
Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.
Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndikuchotsera chokonda maso ako ndi chikomo, koma usamve chisoni, kapena kulira, kapena kudza misozi.
Nena ndi nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzadetsa malo anga opatulika, ulemerero wa mphamvu yanu, chokonda m'maso mwanu, chimene moyo wanu ali nacho chifundo; ndipo ana anu aamuna ndi aakazi otsalira inu adzagwa ndi lupanga.
Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, sikudzakhala kodi tsiku loti ndiwachotsera mphamvu yao, chimwemwe chao chopambana, chowakonda m'maso mwao, ndi chokhumbitsa mtima wao, ana ao aamuna ndi aakazi,
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.
pamene ndinaona pazofunkha malaya abwino a ku Babiloni, ndi masekeli mazana awiri a siliva, ndi chikute chagolide, kulemera kwake masekeli makumi asanu, ndinazikhumbira ndi kuzitenga; ndipo taonani, ndazibisa m'nthaka pakati pa hema wanga, ndi siliva pansi pakepo.
Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.
Ndipo analira pamaso pake masiku asanu ndi awiriwo pochitika madyerero ao; koma kunali kuti tsiku lachisanu ndi chiwiri anamuuza, popeza anamuumiriza; ndipo anatanthauzira anthu a mtundu wake mwambiwo.