Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri ili m'mimba mwako, magulu awiri a anthu adzatuluka m'mimba mwako; gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake; wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.
Genesis 27:8 - Buku Lopatulika Tsopanotu mwana wanga, tamvera mau anga monga momwe nditi ndikuuze iwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsopanotu mwana wanga, tamvera mau anga monga momwe nditi ndikuuze iwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiye iwe mwana wanga, undimvere ndipo uchite zonse zimene ndikuuze. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano mwana wanga, mvetsetsa ndipo uchite zimene ndikuwuze: |
Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri ili m'mimba mwako, magulu awiri a anthu adzatuluka m'mimba mwako; gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake; wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.
Ndipo amake anati kwa iye, Pa ine likhale temberero lako mwana wanga; koma tamvera mau anga, kazimuka kunditengera timeneto.
Ndipo tsopano mwana wanga, tamvera mau anga: tauka, nuthawire kwa Labani mlongo wanga ku Harani;
Unditengere ine nyama, undikonzere ine chakudya chokolera, kuti ndidzadye, ndi kudalitsa iwe pamaso pa Yehova, ndisanafe.
Pitatu kubusa, ukanditengere ine kumeneko tiana tiwiri tabwino tambuzi; ndikonzere nato chakudya chokolera cha atate wako chonga chomwe achikonda:
Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu;