Machitidwe a Atumwi 4:19 - Buku Lopatulika19 Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Koma Petro ndi Yohane adaŵayankha kuti, “Weruzani nokha, kodi pamaso pa Mulungu nkwabwino kumvera inuyo koposa kumvera Mulunguyo? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Koma Petro ndi Yohane anayankha kuti, “Weruzani nokha ngati nʼkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu. Onani mutuwo |
Ndipo mfumu Ahazi analamulira Uriya wansembe, kuti, Paguwa la nsembe lalikulu uzifukiza nsembe yopsereza yam'mawa, ndi nsembe yaufa yamadzulo, ndi nsembe yopsereza ya mfumu, ndi nsembe yake yaufa, pamodzi ndi nsembe yopsereza ya anthu onse a m'dziko, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira; uziwaza pa ilo mwazi wonse wa nsembe yopsereza, ndi mwazi wonse wa nsembe yophera; koma guwa la nsembe lamkuwa ndi langa, lofunsira nalo.