Ndipo nthitiyo anaichotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu.
Genesis 24:44 - Buku Lopatulika ndipo iye akati kwa ine, Imwatu iwe, ndiponso ndidzatungira ngamira zako; yemweyo akhale mkazi amene Yehova wamsankhira mwana wa mbuyanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo iye akati kwa ine, Imwatu iwe, ndiponso ndidzatungira ngamira zako; yemweyo akhale mkazi amene Yehova wamsankhira mwana wa mbuyanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iye akandiyankha kuti: Imwani ndipo ndimwetsanso ngamira zanuzi, ameneyo ndiye akhale namwali amene Chauta wamsankha kuti akhale mkazi wa mwana wa mbuyanga.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo ngati adzandiyankha kuti, ‘Imwani ndipo ndizimwetsanso madzi ngamira zanuzi,’ ameneyo akhale yemwe Yehova wamusankhira mwana wa mbuye wanga.” |
Ndipo nthitiyo anaichotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu.
ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamira zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isaki; ndipo chotero ndidzadziwa kuti mwamchitira mbuyanga ufulu.
taonani, ine ndiima pa kasupe wa madzi, ndipo pakhale, kuti namwali amene atuluka kudzatunga madzi ndimwe pang'ono m'mtsuko mwako;
Ndisanathe kunena m'mtima mwanga, taonani, Rebeka anatuluka ndi mtsuko wake pa phewa lake, natsikira ku kasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu.
Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;