Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 2:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo nthitiyo anaichotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo nthitiyo anaichotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Chauta Mulungu adapanga mkazi ndi nthiti imene adaichotsa kwa Adamu uja, ndipo mkaziyo Mulungu adabwera naye kwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Motero Yehova Mulungu anapanga mkazi ndi nthiti ija imene anatenga kwa munthu uja nabwera naye kwa iye.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 2:22
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m'thengo, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazitcha; ndipo maina omwe onse anazitcha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao.


Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.


Wopeza mkazi apeza chinthu chabwino; Yehova amkomera mtima.


Nyumba ndi chuma ndizo cholowa cha atate; koma mkazi wanzeru achokera kwa Yehova.


Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva;


Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa