Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 24:45 - Buku Lopatulika

45 Ndisanathe kunena m'mtima mwanga, taonani, Rebeka anatuluka ndi mtsuko wake pa phewa lake, natsikira ku kasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

45 Ndisanathe kunena m'mtima mwanga, taonani, Rebeka anatuluka ndi mtsuko wake pa phewa lake, natsikira ku kasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

45 Ndisanamalize nkomwe pemphero langalo, ndinangoona uyu, watulukira Rebeka, atasenza mtsuko pa phewa, akutsikira ku chitsime kudzatunga madzi. Tsono ndinampempha kuti, ‘Chonde patseko madzi ndimwe.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

45 “Ndisanatsirize kupemphera, ndinangoona Rebeka akutulukira mtsuko wake uli pa phewa. Anatsetserekera ku chitsime kukatunga madzi ndipo ndinati kwa iye, ‘Chonde patseko madzi akumwa.’

Onani mutuwo Koperani




Genesis 24:45
14 Mawu Ofanana  

ndipo iye akati kwa ine, Imwatu iwe, ndiponso ndidzatungira ngamira zako; yemweyo akhale mkazi amene Yehova wamsankhira mwana wa mbuyanga.


Pakuti inu, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, munawulula kwa mnyamata wanu kuti, Ndidzakumangira iwe nyumba; chifukwa chake mnyamata wanu analimbika mtima kupemphera pemphero ili kwa Inu.


Ndipo mfumu inati kwa ine, Ufunanji iwe? Pamenepo ndinapemphera Mulungu wa Kumwamba.


Pamenepo udzaitana, ndipo Yehova adzayankha; udzafuula ndipo Iye adzati, Ndine pano. Ngati uchotsa pakati pa iwe goli, kukodolana moipa, ndi kulankhula moipa,


Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.


Ambuye, imvani; Ambuye khululukirani; Ambuye, mverani nimuchite; musachedwa, chifukwa cha inu nokha, Mulungu wanga; pakuti mzinda wanu ndi anthu anu anatchedwa dzina lanu.


Pakuyamba iwe mapembedzero ako, linatuluka lamulo; ndipo ndadza ine kukufotokozera; pakuti ukondedwa kwambiri; zindikira tsono mau awa, nulingirire masomphenyawo.


Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;


Ndipo Kornelio anati, Atapita masiku anai, kufikira monga ora ili, ndinalikupemphera m'nyumba yanga pa ora lachisanu ndi chinai; ndipo taonani, padaimirira pamaso panga munthu wovala chovala chonyezimira,


Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa