inalimbitsidwa kwa Abrahamu ikhale yake, pamaso pa ana a Hiti, pa onse amene analowa pa chipata cha mzinda wake.
Genesis 23:10 - Buku Lopatulika Ndipo Efuroni anakhala pakati pa ana a Hiti, ndipo Efuroni Muhiti anayankha Abrahamu alinkumva ana a Hiti, onse amene analowa pa chipata cha mzinda wake, kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Efuroni anakhala pakati pa ana a Hiti: ndipo Efuroni Muhiti anayankha Abrahamu alinkumva ana a Hiti, onse amene analowa pa chipata cha mudzi wake, kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo nkuti Efuroniyo ali pamodzi ndi Ahiti ku malo ochitirako msonkhano pa chipata cha mudzi. Ndipo anthu onsewo akumva, iye adayankha kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo nʼkuti Efroni Mhiti ali pomwepo pakati pa anthuwo amene anabwera ku chipata cha mzindawo. Ndipo onse akumva anamuyankha Abrahamu |
inalimbitsidwa kwa Abrahamu ikhale yake, pamaso pa ana a Hiti, pa onse amene analowa pa chipata cha mzinda wake.
kuti andipatse ine phanga la Makipela, limene lili pansonga pamunda wake; pa mtengo wake wonse andipatse pakati pa inu, ndikhale nao manda.
Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
Ndipo Hamori ndi Sekemu mwana wake anafika ku chipata cha mzinda wao, nalankhulana ndi anthu a mzinda wao, kuti,
Ndipo onse amene anatuluka pa chipata cha mzinda wao anamvera Hamori ndi mwana wake Sekemu, nadulidwa amuna onse akutuluka pa chipata cha mzinda wao.
ndipo adzakhala mzimu wa chiweruziro kwa oweruza milandu, ndi mphamvu kwa iwo amene abweza nkhondo pachipata.
Pamenepo anthu onse anali kuchipata, ndi akulu, anati, Tili mboni ife. Yehova achite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israele, iwo awiri; nuchite iwe moyenera mu Efurata, numveke mu Betelehemu;