Rute 4:11 - Buku Lopatulika11 Pamenepo anthu onse anali kuchipata, ndi akulu, anati, Tili mboni ife. Yehova achite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israele, iwo awiri; nuchite iwe moyenera mu Efurata, numveke mu Betelehemu; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Pamenepo anthu onse anali kuchipata, ndi akulu, anati, Tili mboni ife. Yehova achite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israele, iwo awiri; nuchite iwe moyenera m'Efurata, numveke m'Betelehemu; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Apo anthu onse amene anali pachipata paja, pamodzi ndi atsogoleri aja, adati, “Inde, ndife mboni. Mkazi amene akudzaloŵa m'nyumba mwakoyo, Chauta amsandutse wofanafana ndi Rakele ndi Leya, akazi amene adamanga banja la Israele pombalira ana ambiri. Ukhale munthu wosasoŵa kanthu mu mzinda wa Efurata, ndipo ukhale munthu wotchuka mu mzinda wa Betelehemu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Ndipo akuluakulu aja ndi anthu onse amene anali pa chipata anati, “Ife ndife mboni, ndipo Yehova amusandutsa mkazi amene akudzalowa mʼnyumba yakoyu kuti akhale ngati Rakele ndi Leya, amene anamanga banja la Israeli. Ukhale munthu wosasowa kanthu mu Efurata ndi munthu wotchuka mu Betelehemu. Onani mutuwo |