Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Rute 4:12 - Buku Lopatulika

12 ndi nyumba yako inge nyumba ya Perezi, amene Tamara anambalira Yuda, ndi mbeu imene Yehova adzakupatsa ya namwali uyu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 ndi nyumba yako inge nyumba ya Perezi, amene Tamara anambalira Yuda, ndi mbeu imene Yehova adzakupatsa ya namwali uyu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ana ako amene Chauta adzakupatse mwa mai ameneyu, adzamange banja longa la Perezi, amene Tamara adabalira Yuda.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ana amene Yehova adzakupatsa mwa mkaziyu adzamange banja lako kukhala la Perezi, amene Tamara anamubalira Yuda.”

Onani mutuwo Koperani




Rute 4:12
8 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene iye anabweza dzanja lake, kuti, taona, mbale wake anabadwa, ndipo namwino anati, Wadziphothyolera wekha bwanji? Chifukwa chake dzina lake linatchedwa Perezi.


Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.


Ndi Tamara mpongozi wake anambalira Perezi ndi Zera. Ana aamuna onse a Yuda ndiwo asanu.


Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense.


ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu;


Iyo ndiyo mibadwo ya Perezi; Perezi anabala Hezironi;


Ndipo Eli anadalitsa Elikana ndi mkazi wake, nati, Yehova akupatse mbeu ndi mkazi uyu m'malo mwa iye amene munampempha kwa Yehova. Ndipo iwowa anabwera kwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa