Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 34:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo onse amene anatuluka pa chipata cha mzinda wao anamvera Hamori ndi mwana wake Sekemu, nadulidwa amuna onse akutuluka pa chipata cha mzinda wao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo onse amene anatuluka pa chipata cha mudzi wao anamvera Hamori ndi mwana wake Sekemu, nadulidwa amuna onse akutuluka pa chipata cha mudzi wao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Anthu amumzindamo adavomereza zimene Hamori ndi Sekemu adanena, ndipo amuna onse amumzindamo adaumbalidwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Amuna onse amene anatuluka ku chipata cha mzinda anavomerezana ndi Hamori ndi mwana wake Sekemu, ndipo aliyense wamwamuna mu mzindamo anachita mdulidwe.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 34:24
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anatenga Ismaele mwana wake ndi onse amene anabadwa m'nyumba mwake, ndi onse amene anagulidwa ndi ndalama zake, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwake kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye.


Ndipo Efuroni anakhala pakati pa ana a Hiti, ndipo Efuroni Muhiti anayankha Abrahamu alinkumva ana a Hiti, onse amene analowa pa chipata cha mzinda wake, kuti,


inalimbitsidwa kwa Abrahamu ikhale yake, pamaso pa ana a Hiti, pa onse amene analowa pa chipata cha mzinda wake.


Kodi ng'ombe zao ndi chuma chao ndi zoweta zao sizidzakhala zathu? Pokhapo tivomerezana nao ndipo adzakhala pamodzi ndi ife.


Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.


Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusunga kwa malamulo a Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa