Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 23:9 - Buku Lopatulika

9 kuti andipatse ine phanga la Makipela, limene lili pansonga pamunda wake; pa mtengo wake wonse andipatse pakati pa inu, ndikhale nao manda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 kuti andipatse ine phanga la Makipela, limene lili pansonga pa munda wake; pa mtengo wake wonse andipatse pakati pa inu, ndikhale nao manda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 kuti andigulitse phanga la Makipera ali naloli. Phangalo lili m'malire a munda wake. Mpempheni kuti andigulitse pa mtengo wake ndithu, inu mukupenya, kuti malowo ndiŵasandutse manda.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 kuti andigulitse phanga la Makipela, limene lili kumapeto kwa munda wake. Mumupemphe kuti andigulitse pamtengo wake ndithu inu mukuona kuti akhale manda.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 23:9
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Efuroni anakhala pakati pa ana a Hiti, ndipo Efuroni Muhiti anayankha Abrahamu alinkumva ana a Hiti, onse amene analowa pa chipata cha mzinda wake, kuti,


Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso.


Ndipo ananena nao, kuti, Ngati mukandivomereza kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso, mundimvere ine, mundinenere ine kwa Efuroni mwana wake wa Zohari,


munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Hiti. Pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wake.


Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanitsidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m'phanga lili m'munda wa Efuroni Muhiti,


chifukwa kuti ana ake aamuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efuroni Muhiti, patsogolo pa Mamure.


Davide tsono anati kwa Orinani, Ndipatse padwale pano kuti ndimangepo guwa la nsembe la Yehova; undipatse ili pa mtengo wake wonse, kuti mliri ulekeke pa anthu.


Koma mfumu Davide anati kwa Orinani, Iai, koma ndidzaligula pa mtengo wake wonse; pakuti sindidzatengera Yehova chili chako, kapena kupereka nsembe yopsereza yopanda mtengo wake.


Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.


Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa