Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 22:23 - Buku Lopatulika

Ndimo Betuele anabala Rebeka: amenewa asanu ndi atatu Milika anambalira Nahori mphwake wa Abrahamu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndimo Betuele anabala Rebeka: amenewa asanu ndi atatu Milika anambalira Nahori mphwake wa Abrahamu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Betuele adabereka Rebeka. Milika adabalira Nahori mbale wa Abrahamu ana asanu ndi atatu ameneŵa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Betueli anabereka Rebeka. Milika anaberekera Nahori, mʼbale wake wa Abrahamu, ana aamuna asanu ndi atatu amenewa.

Onani mutuwo



Genesis 22:23
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lake la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lake la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wake wa Harani, atate wake wa Milika, ndi atate wake wa Isika.


ndi Kesedi, ndi Hazo, ndi Pilidasi ndi Yidilafi, ndi Betuele.


Ndipo mkazi wake wamng'ono, dzina lake Reuma, iyenso anabala Teba, ndi Gahamu, ndi Tahasi, ndi Maaka.


Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.


Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Ine ndine mwana wa Betuele mwana wamwamuna wa Milika, amene anambalira Nahori.


Ndipo ndinamfunsa iye kuti, Ndiwe mwana wa yani kodi? Ndipo anati, Ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori amene anambalira iye Milika: ndipo ndinaika mphete pambuyo pake ndi zingwinjiri pa manja ake.


Taonani, Rebeka ali pamaso pako, mtenge ndi kumuka, akhale mkazi wa mwana wa mbuyako, monga wanena Yehova.


Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao.


Ndipo Isaki anamlowetsa mkaziyo m'hema wa amake Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wake; ndipo anamkonda iye; ndipo Isaki anatonthozedwa mtima atafa amake.


ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.


Tauka, nupite ku Padanaramu, kunyumba ya Betuele, atate wa amai ako; ukadzitengere mkazi wa kumeneko kwa ana aakazi a Labani mlongo wake wa amai ako.


Ndipo Isaki anamlola Yakobo amuke, ndipo ananka ku Padanaramu kwa Labani, mwana wake wa Betuele Mwaramu, mlongo wake wa Rebeka, amai wao wa Yakobo ndi Esau.


Ndipo si chotero chokha, koma Rebekanso, pamene anali ndi pakati pa mmodzi, ndiye kholo lathu Isaki;