Dzina la woyamba ndi Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m'mene muli golide;
Genesis 2:12 - Buku Lopatulika golide wa dziko ali wabwino; ndimonso muli bedola ndi mwala wasohamu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 golide wa dziko ali wabwino; ndimonso muli bedola ndi mwala wasohamu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa (Golide wakumeneko ndi wabwino. Kumapezekanso bedeliyo ndi miyala ya mtengowapatali yotchedwa onikisi.) Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Golide wa ku dziko ili ndi wabwino. Kulinso miyala yokongola ya bedola ndi onikisi). |
Dzina la woyamba ndi Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m'mene muli golide;
ndi mzere wachinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; zikhale zogwirika ndi golide m'zoikamo zao.
Ndi mzere wachinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; inakhala yogwirika ndi golide maikidwe ake.
Unali mu Edeni, munda wa Mulungu, mwala uliwonse wa mtengo wake unali chofunda chako, sardiyo, topazi, diamondi, berulo, sohamu, ndi yaspi, safiro, nofeki, bareketi, ndi golide; malingaka ako ndi akazi ako anakutumikira tsiku lolengedwa iwe zinakonzekeratu.