Genesis 16:1 - Buku Lopatulika Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu sanambalire iye mwana; ndipo anali ndi mdzakazi, wa ku Ejipito, dzina lake Hagara. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu sanambalire iye mwana; ndipo anali ndi mdzakazi, wa ku Ejipito, dzina lake Hagara. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sarai mkazi wa Abramu, sadam'balire ana Abramuyo. Koma Sarai anali ndi mdzakazi wake wa ku Ejipito dzina lake Hagara. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Sarai, mkazi wa Abramu anali asanamuberekere ana Abramuyo. Koma anali ndi wantchito wamkazi wa ku Igupto dzina lake Hagara; |
Ndipo anamchitira Abramu bwino chifukwa cha iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi abulu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi abulu aakazi, ndi ngamira.
Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Usaipidwe nao, chifukwa cha mnyamatayo, ndi chifukwa cha mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mau ake; chifukwa kuti mwa Isaki zidzaitanidwa mbeu zako.
Ndipo anakhala m'chipululu cha Parani; ndipo amake anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Ejipito.
Ndipo Isaki anampembedzera mkazi wake kwa Yehova popeza anali wouma: ndipo Yehova analola kupembedza kwake, ndipo Rebeka mkazi wake anatenga pakati.
Ndipo taona, Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma.
pakuti akaziwa ali mapangano awiri, mmodzi wa kuphiri la Sinai, akubalira ukapolo, ndiye Hagara.
Ndipo panali munthu wina wa Zora wa banja la Adani, dzina lake ndiye Manowa; ndi mkazi wake analibe mwana, sanabale.
koma anapatsa Hana magawo awiri, chifukwa anakonda Hana, koma Yehova anatseka mimba yake.