Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 1:36 - Buku Lopatulika

36 Ndipo taona, Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Ndipo taona, Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna m'ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 “Onani, mbale wanu uja Elizabeti, nayenso akuyembekezera mwana wamwamuna mu ukalamba wake. Anthu amati ngwosabala, komabe uno ndi mwezi wake wachisanu ndi chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Ngakhale Elizabeti mʼbale wako adzakhala ndi mwana mu ukalamba wake ndipo iye amene amati ndi wosabereka, uno mwezi wake wachisanu ndi chimodzi.

Onani mutuwo Koperani




Luka 1:36
10 Mawu Ofanana  

Koma Sarai anali wouma; analibe mwana.


Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu sanambalire iye mwana; ndipo anali ndi mdzakazi, wa ku Ejipito, dzina lake Hagara.


Koma Abrahamu ndi Sara anali okalamba, anapitirira masiku ao; ndipo kunaleka kwa Sara konga kumachita ndi akazi;


Ndipo Sara anatenga pakati, nambalira Abrahamu mu ukalamba wake mwana wamwamuna, nthawi yomweyo Mulungu anamuuza iye.


Ndipo mkaziyo anaima, naona mwana wamwamuna nyengo yomweyo chaka chimene chija Elisa adanena naye.


mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo;


Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.


Chifukwa palibe mau amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.


Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana aakazi a fuko la Aroni, dzina lake Elizabeti.


Ndi chikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yake, popeza anamwerengera wokhulupirika Iye amene adalonjeza;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa