Dziko lonse silili pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukanka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndinka ku dzanja lamanja: ukanka iwe ku dzanja lamanja, ine ndinka ku dzanja lamanzere.
Genesis 13:8 - Buku Lopatulika Ndipo Abramu anati kwa Loti, Tisachite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abramu anati kwa Loti, Tisachite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Abramu adauza Loti kuti, “Ifetu ndife abale, choncho pasakhale kukangana pakati pa iwe ndi ine, ndipo abusa ako sayenera kumakangana ndi abusa anga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Abramu anati kwa Loti, “Pasakhale mikangano pakati pa iwe ndi ine kapena pakati pa abusa ako ndi anga, popeza ndife abale. |
Dziko lonse silili pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukanka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndinka ku dzanja lamanja: ukanka iwe ku dzanja lamanja, ine ndinka ku dzanja lamanzere.
Pamene anamva Abramu kuti mphwake anagwidwa, anatuluka natsogolera anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kufikira ku Dani.
Mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng'ombe chiyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m'dziko la Goseni; chifukwa abusa onse anyansira Aejipito.
M'mawa mwake anatulukanso, ndipo, taonani, anthu awiri Ahebri alikumenyana; ndipo ananena ndi wochimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako?
Ndipo m'mawa mwake anawaonekera alikulimbana ndeu, ndipo anati awateteze, ayanjanenso, nati, Amuna inu, muli abale; muchitirana choipa bwanji?
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
Koma kunena za chikondano cha pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzake;
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:
Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima;
Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;
koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo;
Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu.
Ndipo Gaala, mwana wa Ebedi anadza ndi abale ake, napita ku Sekemu; ndi eni ake a ku Sekemu anamkhulupirira.