Amenewo ndipo anagawa zisumbu za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.
Genesis 10:6 - Buku Lopatulika Ndi ana aamuna a Hamu: Kusi, ndi Ejipito, ndi Puti, ndi Kanani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi ana amuna a Hamu: Kusi, ndi Ejipito, ndi Puti, ndi Kanani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana a Hamu anali Kusi, Ejipito, Libia ndi Kanani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana aamuna a Hamu anali: Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani. |
Amenewo ndipo anagawa zisumbu za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.
Ndi ana aamuna a Nowa amene anatuluka m'chingalawa ndiwo Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti. Hamu ndiye atate wake wa Kanani.
Ndipo Hamu atate wake wa Kanani, anauona umaliseche wa atate wake, nauza abale ake awiri amene anali kunja.
Ndipo anapeza podyetsa ponenepetsa ndi pabwino, ndipo dzikoli ndi lachitando ndi lodikha ndi losungikamo, pakuti okhalako kale ndiwo a Hamu.
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja.
Kwerani, inu akavalo; chitani misala, inu magaleta, atuluke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira chikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta.
Apersiya, Aludi, Aputi, anali m'khamu lako; anthu ako a nkhondo anapachika chikopa ndi chisoti mwa iwe, anamveketsa kukoma kwako.