Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 9:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo Hamu atate wake wa Kanani, anauona umaliseche wa atate wake, nauza abale ake awiri amene anali kunja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo Hamu atate wake wa Kanani, anauona umaliseche wa atate wake, nauza abale ake awiri amene anali kunja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Hamu, bambo wake wa Kanani, ataona kuti Nowa bambo wake ali maliseche, adapita nakauza abale ake aŵiri aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Hamu, abambo ake a Kanaani ataona kuti abambo ake ali maliseche anakawuza abale ake awiri aja omwe anali panja.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 9:22
17 Mawu Ofanana  

Ndi ana aamuna a Hamu: Kusi, ndi Ejipito, ndi Puti, ndi Kanani.


Semu ndi Yafeti ndipo anatenga chofunda, nachiika pa mapewa ao a onse awiri, nayenda chambuyo, nafunditsa umaliseche wa atate wao: nkhope zao zinali chambuyo, osaona umaliseche wa atate ao.


Ndipo anati, Wotembereredwa ndi Kanani; adzakhala kwa abale ake kapolo wa akapolo.


Ana a Hamu: Kusi, ndi Ejipito, Puti, ndi Kanani.


Apululuke, mobwezera manyazi ao amene anena nane, Hede, hede.


Abwerere, kukhale mphotho ya manyazi ao amene akuti, Hede, hede.


Nena mlandu wako ndi mnzako, osawulula zinsinsi za mwini;


Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makwangwala a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.


Tsoka wakuninkha mnzake chakumwa, ndi kuonjezako mankhwala ako, ndi kumledzeretsa, kuti upenyerere manyazi ao!


Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.


sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi;


Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa