Genesis 10:15 - Buku Lopatulika Ndipo Kanani anabala Sidoni woyamba wake, ndi Heti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Kanani anabala Sidoni woyamba wake, ndi Heti: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kanani adabereka mwana wake wachisamba dzina lake Sidoni, ndipo adaberekanso Heti. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kanaani anabereka mwana wake wachisamba, Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti; |
ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Zebuloni adzakhala m'mphepete mwa nyanja; ndipo iye adzakhala dooko la ngalawa; ndipo malire ake adakhala pa Sidoni.
Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu, mkazi wa Uriya Muhiti?
nafika ku Giliyadi ndi ku dera la Tatimuhodisi; nafika ku Dani-Yaana ndi kuzungulira, kufikira ku Sidoni,
ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.
Dzisungire chimene Ine ndikuuza lero lino: taona, ndiingitsa pamaso pako Aamori ndi Akanani, ndi Ahiti ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.
Khala ndi manyazi, iwe Sidoni; chifukwa nyanja yanena, linga la kunyanja, ndi kuti, Ine sindinamve zowawa, kapena kubala, kapena kulera anyamata, kapena kulera anamwali.
chifukwa cha tsiku lakudzafunkha Afilisti onse, kuphera Tiro ndi Sidoni othangata onse akutsala; pakuti Yehova adzafunkha Afilisti, otsala a chisumbu cha Kafitori.
Okhala mu Sidoni ndi Arivadi ndiwo opalasa ako; anzeru ako, Tiro, okhala mwa iwe, ndiwo oongolera ako.
Ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Israele, ndipo anawakantha, nawapirikitsa mpaka ku Sidoni waukulu, ndi ku Misirefoti-Maimu, ndi ku chigwa cha Mizipa ku m'mawa; nawakantha mpaka sanawasiyire ndi mmodzi yense.
Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Muhiti, ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wake wa Yowabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Saulo? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.