Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 11:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Israele, ndipo anawakantha, nawapirikitsa mpaka ku Sidoni waukulu, ndi ku Misirefoti-Maimu, ndi ku chigwa cha Mizipa ku m'mawa; nawakantha mpaka sanawasiyire ndi mmodzi yense.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Israele, ndipo anawakantha, nawapirikitsa mpaka ku Sidoni waukulu, ndi ku Misirefoti-Maimu, ndi ku chigwa cha Mizipa ku m'mawa; nawakantha mpaka sanawasiyire ndi mmodzi yense.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Chauta adapatsa Aisraelewo mphamvu zogonjetsera adaniwo, mwakuti adaŵapambana kwenikweni, naŵapirikitsa mpaka kumpoto ku Sidoni Wamkulu ndi ku Misirefoti-Maimu ndiponso kuvuma, ku chigwa cha Mizipa. Adapha onsewo, osatsala ndi mmodzi yemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Yehova anawapereka mʼmanja mwa Israeli mwakuti anawagonjetseratu ndi kuwapirikitsa njira yonse mpaka ku Sidoni Wamkulu ndi ku Misirefoti Maimu, ndiponso kummawa ku chigwa cha Mizipa. Onse anaphedwa popanda wopulumuka.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 11:8
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Kanani anabala Sidoni woyamba wake, ndi Heti,


Zebuloni adzakhala m'mphepete mwa nyanja; ndipo iye adzakhala dooko la ngalawa; ndipo malire ake adakhala pa Sidoni.


nafika ku Giliyadi ndi ku dera la Tatimuhodisi; nafika ku Dani-Yaana ndi kuzungulira, kufikira ku Sidoni,


Khala ndi manyazi, iwe Sidoni; chifukwa nyanja yanena, linga la kunyanja, ndi kuti, Ine sindinamve zowawa, kapena kubala, kapena kulera anyamata, kapena kulera anamwali.


ndi Hamati yemwe wogundana naye malire; Tiro ndi Sidoni, angakhale ali ndi nzeru zambiri.


nakawapereka Yehova Mulungu wanu pamaso panu, ndipo mukawakanthe; pamenepo muwaononge konse; musapangana nao pangano, kapena kuwachitira chifundo.


Potero mudziwe lero lino, kuti Yehova Mulungu wanu ndiye amene aoloka pamaso panu ngati moto wonyeketsa; Iye adzawaononga, Iye adzawagwetsa pamaso panu; potero mudzawapirikitsa, ndi kuwaononga msanga, monga Yehova analankhula ndi inu.


Ndipo kunali, Yoswa ndi ana a Israele atatha kuwakantha, makanthidwe aakulukulu mpaka atatha psiti, ndipo otsala a iwo atalowa m'mizinda ya malinga,


kwa Akanani kum'mawa ndi kumadzulo, ndi kwa Aamori ndi Ahiti, ndi Aperizi ndi Ayebusi kumapiri, ndi kwa Ahivi kunsi kwa Heremoni, m'dziko la Mizipa.


Ndipo Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo naye, anawadzera modzidzimutsa ku madzi a Meromu, nawagwera.


nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebanoni, mpaka Misirefoti-Maimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israele, koma limeneli uwagawire Aisraele, likhale cholowa chao, monga ndinakulamulira.


ndi Ebroni, ndi Rehobu, ndi Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkulu;


Ndipo Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse, monga mwa zonse adalumbirira makolo ao; ndipo pamaso pao sipanaime munthu mmodzi wa adani ao onse; Yehova anapereka adani ao onse m'manja mwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa