Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabwino; ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima.
Genesis 1:10 - Buku Lopatulika Ndipo Mulungu adautcha mtundawo Dziko lapansi; kusonkhana kwa madziko ndipo adatcha Nyanja: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mulungu adautcha mtundawo Dziko lapansi; kusonkhana kwa madziko ndipo adatcha Nyanja: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu adautcha mtundawo Dziko, madzi adaŵasonkhanitsa aja adaŵatcha Nyanja. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabwino; ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima.
Amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'mwemo. Ndiye wakusunga choonadi kosatha,
Ndipo ananena nao, Ndine Muhebri, ndiopa Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda.
Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.