Genesis 1:11 - Buku Lopatulika11 Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere udzu, therere lobala mbeu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wake, momwemo muli mbeu yake, padziko lapansi: ndipo kunatero. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere udzu, therere lobala mbeu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wake, momwemo muli mbeu yake, pa dziko lapansi: ndipo kunatero. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Tsono adati, “Panthaka pamere zomera zobala njere, ndiponso mitengo yobala zipatso zanjere malinga ndi mtundu wake,” ndipo zidachitikadi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Kenaka Mulungu anati, “Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi. Onani mutuwo |